Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Genesis 5 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is the written record of Adam's descendants. When our Father created humankind, he made them in the likeness of God. Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu.
2 He created them male and female, blessed them, and named them Humankind when they were created. Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
3 At 130, Adam fathered a son in his likeness, after his image, and named him Seth. Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
4 After he fathered Seth, Adam lived 800 years and had other sons and daughters. Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
5 Altogether, Adam lived 930 years, and then he died. Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
6 When Seth had lived 105 years, he fathered Enosh. Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi.
7 After he fathered Enosh, Seth lived 807 years and had other sons and daughters. Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
8 Altogether, Seth lived 912 years, and then he died. Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
9 When Enosh had lived ninety years, he fathered Kenan. Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani.
10 After he fathered Kenan, Enosh lived 815 years and had other sons and daughters. Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
11 Altogether, Enosh lived 905 years, and then he died. Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
12 When Kenan had lived seventy years, he fathered Mahalalel. Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli.
13 After he fathered Mahalalel, Kenan lived 840 years and had other sons and daughters. Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
14 Altogether, Kenan lived 910 years, and then he died. Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
15 When Mahalalel had lived sixty-five years, he fathered Jared. Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.
16 After he fathered Jared, Mahalalel lived 830 years and had other sons and daughters. Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
17 Altogether, Mahalalel lived 895 years, and then he died. Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
18 When Jared had lived 162 years, he fathered Enoch. Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki.
19 After he fathered Enoch, Jared lived 800 years and had other sons and daughters. Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
20 Altogether, Jared lived 962 years, and then he died. Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
21 When Enoch had lived sixty-five years, he fathered Methuselah. Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela.
22 After fathering Methuselah, Enoch walked with our Father 300 years, and had other sons and daughters. Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
23 Altogether, Enoch lived 365 years. Zaka zonse za Enoki zinali 365.
24 Enoch walked faithfully with our Father; then he was gone, because our Father took him. Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
25 When Methuselah had lived 187 years, he fathered Lamech. Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki.
26 After he fathered Lamech, Methuselah lived 782 years and had other sons and daughters. Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
27 Altogether, Methuselah lived 969 years, and then he died. Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
28 When Lamech had lived 182 years, he fathered a son. Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.
29 He named him Noah, saying, "He will comfort us in our work and painful toil of our hands, from the ground our Father cursed." Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.”
30 After he fathered Noah, Lamech lived 595 years and had other sons and daughters. Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi.
31 Altogether, Lamech lived 777 years, and then he died. Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
32 When Noah was 500 years old, he fathered Shem, Ham, and Japheth. Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]