Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Ezra 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 In the seventh month, with Israel settled in their towns, the people gathered as one in Jerusalem. Utafika mwezi wa chisanu ndi chiwiri Aisraeli atakhala kale mʼmidzi yawo, anthu anasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi.
2 Then Jeshua son of Jozadak and his fellow priests, and Zerubbabel son of Shealtiel and his associates, set to work and built the altar of our Father, to offer burnt offerings on it, as it is written in the Law of Moses, the man of our Father. Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja.
3 They set the altar on its foundations, fearing the peoples around them, and offered burnt offerings on it to our Father morning and evening. Ndi mantha ndi mantha chifukwa cha anthu a mʼmayikomo, iwo anamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu pa guwapo mmawa ndi madzulo.
4 They kept the Feast of Booths as written, the daily burnt offerings in the number each day required. Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.
5 After that, they offered the regular burnt offerings, the new moon offerings, all our Father's sacred feasts, and gifts from anyone who brought a voluntary offering to our Father. Pambuyo pake, ankapereka nsembe zopsereza, nsembe zopereka pa nthawi ya mwezi watsopano ndi za pa masiku onse a chikondwerero oyikidwa kutamandira Yehova, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Yehova.
6 From the first day of the seventh month, they began offering burnt offerings to our Father, though our Father's temple foundation was not yet laid. Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
7 They paid masons and carpenters, and gave the Sidonians and Tyrians food, drink, and oil, to bring cedar logs from Lebanon by sea to Joppa, as Cyrus king of Persia had authorized them. Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
8 In the second month of year two after they reached our Father's house in Jerusalem, Zerubbabel son of Shealtiel and Jeshua son of Jozadak began the work, with the rest of their people—the priests, the Levites, and all who'd returned to Jerusalem from captivity. They set Levites twenty and older over the work on our Father's house. Tsono mu chaka chachiwiri atabwera ku Yerusalemu, ku malo akale a Nyumba ya Yehova, mwezi wachiwiri Zerubabeli mwana wa Sealatieli, Yesuwa mwana wa Yozadaki pamodzi ndi abale awo onse, ansembe, Alevi ndi onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo, anayamba kugwira ntchito. Iwo anasankha Alevi a zaka zoyambira makumi awiri kuti aziyangʼanira ntchito ya kumanga Nyumba ya Yehova.
9 Then Jeshua, his sons and brothers, and Kadmiel with his sons, sons of Judah, joined together to oversee those working on our Father's house—along with Henadad's sons, their sons and brothers, the Levites. Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
10 When the builders laid the foundation of our Father's temple, priests in robes stood with trumpets, and Levites, sons of Asaph, with cymbals, to praise our Father as David king of Israel had ordered. Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli.
11 They sang responsively, praising and thanking our Father: "He is good; his faithful love for Israel lasts forever." All the people gave a great shout of praise, because the foundation of our Father's house was laid. Iwo ankayimba motamanda ndi mothokoza Yehova nyimbo iyi: “Yehova ndi wabwino; chikondi chake pa Israeli ndi chamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuwula kwambiri kumutamanda Yehova, chifukwa maziko a Nyumba ya Yehova anali kumangidwa.
12 Many older priests, Levites, and clan heads who had seen the first house wept loudly as this house's foundation was laid before their eyes, while many others shouted for joy. Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala.
13 No one could distinguish the joyful shout from the weeping, since the people shouted so loudly it was heard far off. Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]