Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Esther 3 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 After this King Xerxes promoted Haman son of Hammedatha the Agagite, elevating him and raising his seat above all the officials with him. Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse.
2 All the king's servants at the king's gate knelt and bowed to Haman, as the king ordered. But Mordecai would not kneel or bow. Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.
3 So the king's servants at the king's gate asked Mordecai, "Why do you disobey the king's command?" Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?”
4 Day after day they urged him, but he refused; so they told Haman, to see if Mordecai's stand would hold, since he had told them he was a Jew. Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda.
5 When Haman saw that Mordecai would not kneel or bow to him, he was filled with rage. Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri.
6 Killing only Mordecai seemed beneath him, since they had told him who Mordecai's people were; so Haman sought to destroy all Mordecai's people, the Jews, throughout Xerxes's kingdom. Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira.
7 In the first month, Nisan, in King Xerxes's twelfth year, they cast Pur (the lot) before Haman for each day and each month; and the lot fell on the twelfth month, Adar. Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.
8 Haman told King Xerxes, "A certain people is scattered and dispersed among the peoples throughout your kingdom's provinces. Their laws differ from everyone's, and they ignore the king's laws; it profits the king nothing to tolerate them. Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere.
9 If it pleases the king, let it be written to destroy them; I'll weigh 375 tons of silver to his officials for the royal treasury." Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.”
10 The king took off his signet ring and gave it to Haman son of Hammedatha the Agagite, enemy of the Jews. Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda.
11 "The silver is yours," the king told Haman, "and the people too—do with them as you please." Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.”
12 On the first month's thirteenth day the king's scribes were summoned, and Haman's order was written to the king's satraps, the governors over each province, and the officials of every people—each province in its own script, each people its own language. Written in King Xerxes's name, sealed with his signet ring. Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake.
13 Couriers carried letters to all the king's provinces: destroy, kill, and eliminate all Jews—young and old, women and children—in one day, thirteenth of the twelfth month, Adar, and seize their goods. Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo.
14 A copy was to be issued as law in every province, shown to all peoples, so they would be ready for that day. Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo.
15 At the king's command couriers rushed out, and the decree went out in the fortress of Susa. The king and Haman sat drinking, but the city of Susa was bewildered. Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]