Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Deuteronomy 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Then we turned and traveled toward the wilderness by way of the Red Sea, as our Father told me, and circled Mount Seir for many days. Kenaka tinabwerera ndi kuyamba ulendo wolowera ku chipululu motsatira njira ya ku Nyanja Yofiira, monga mmene Yehova anatilamulira. Kwa nthawi yayitali tinayendayenda cha ku dziko la mapiri la Seiri.
2 Then our Father said to me, Ndipo Yehova anati kwa ine,
3 "You have gone around this hill country long enough. Turn northward. “Mwazungulira mokwanira dziko la mapiri, tsopano tembenukirani kumpoto.
4 Command the people: You are crossing the territory of your brothers, Esau's descendants, who live in Seir. They will fear you—be very careful. Apatse anthu malamulo awa: ‘Muli pafupi kudutsa mʼchigawo cha abale anu adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Iwowa adzachita nanu mantha koma musamale kwambiri.
5 Do not provoke them; I will not give you any of their land, not even a footstep's width, since I have given Mount Seir to Esau as his possession. Musayambane nawo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo ngakhale poti mungoyika phazi. Ndamupatsa Esau dziko lamapiri la Seiri kuti likhale lakelake.
6 Buy food from them for silver to eat, and also buy water from them for silver to drink. Inu muyenera kuwalipira ndi siliva pa chakudya chimene mudye ndi madzi amene mumwe.’ ”
7 "For your Father has blessed you in all the work of your hands. He has known your journey through this great wilderness. These forty years your Father has been with you; you have lacked nothing." Yehova Mulungu wanu wakudalitsani mʼntchito zonse za manja anu. Iye wakuyangʼanirani pa ulendo wanu wodutsa mʼchipululu chachikulu. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu mʼzaka makumi anayi, ndipo simunasowe kalikonse.
8 So we passed by our brothers, the descendants of Esau who live in Seir, away from the Arabah road that comes up from Elath and Ezion-geber. Then we turned and went on toward the wilderness of Moab. Choncho tinapitiriza ulendo modutsa abale athu, adzukulu a Esau okhala ku Seiri. Tinapatukira njira ya ku Araba imene imachokera ku Elati ndi Ezioni Geberi ndipo tinayenda njira ya ku chipululu cha Mowabu.
9 And our Father said to me, "Do not harass Moab or provoke them to battle, for I will not give you any of their land as a possession, since I have given Ar to Lot's descendants as a possession." Ndipo Yehova anati kwa ine, “Musawavutitse Amowabu kapena kuwaputa kuti muchite nawo nkhondo popeza sindidzakupatsani gawo lina lililonse la dziko lawo. Ndinapereka Ari kwa adzukulu a Loti ngati chuma chawo.”
10 (The Emim formerly lived there, a large and powerful people, as tall as the Anakim. (Aemi, anthu amphamvu ndi ochuluka komanso ataliatali ngati Aanaki amakhala kumeneko.
11 Like the Anakim, they too are counted as Rephaim, but the Moabites call them Emim. Ngati Aanaki, nawonso ankawayesa kuti anali Arefai, koma Amowabu ankawatcha iwo Aemi.
12 Horites once lived in Seir, but Esau's descendants drove out and destroyed them, settling in their place—just as Israel did in the land our Father gave them.). Ahori amakhala ku Seiri koma adzukulu a Esau anawapirikitsa. Iwo anawononga Ahori pamaso pawo nawakhalira pamalo pawo monga Aisraeli anachitira mʼdziko limene Yehova anawapatsa ngati chuma chawo).
13 Now get moving and cross the Wadi Zered." So we crossed the Wadi Zered. Ndipo Yehova anati, “Tsopano nyamukani ndipo muwoloke Chigwa cha Zeredi.” Choncho tinawoloka chigwacho.
14 From Kadesh-barnea to crossing the Wadi Zered took thirty-eight years, until the whole generation of fighting men had died out of the camp, as our Father had sworn to them. Panapita zaka 38 kuchokera pa nthawi imene tinachoka ku Kadesi Barinea mpaka pamene tinawoloka Chigwa cha Zeredi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mʼbado wonse wa anthu ankhondowo utawonongeka ku msasa monga Yehova anawalumbirira.
15 Indeed, the hand of our Father was against them, rooting them out from the camp until they perished. Dzanja la Yehova linatsutsana nawo mpaka wonse anathera ku msasa.
16 So when all the fighting men had finally perished and died from among the people, Tsono atafa munthu wotsiriza mwa anthu ankhondowo,
17 our Father said to me, Yehova anati kwa ine,
18 "Today you are to cross the boundary of Moab at Ar. “Lero mudutsa malire a Mowabu ku Ari podzera ku Ari.
19 When you come near the Ammonites, do not attack or provoke them, for I will not give you any of their land as a possession—I gave it to Lot's descendants as their possession." Mukafika kwa Aamoni, musawavutitse kapena kuwaputa, popeza sindidzakupatsani gawo lililonse la dziko la Aamoni. Ine ndalipereka dzikoli ngati chuma kwa adzukulu a Loti.”
20 (That too counts as Rephaim land—Rephaim lived there before, though Ammonites call them Zamzummim, (Ilinso ankaliyesa dziko la Arefai amene ankakhala kumeneko. Koma Aamoni ankawatcha iwo Azamuzumi.
21 a large and powerful people, tall as the Anakim. But our Father destroyed them before the Ammonites, who drove them out and settled in their place, Iwo anali anthu amphamvu ndiponso ochuluka, ataliatali ngati Aanaki. Yehova anawawononga ndi kuwachotsa pamaso pa Aamoni, amene anawapirikitsa nawakhalira pa malo pawo.
22 as he did for Esau's descendants living in Seir, when he destroyed the Horites before them; they drove them out and settled in their place, remaining to this day. Yehova anachitanso chimodzimodzi ndi adzukulu a Esau omwe anakhazikika ku Seiri atawononga Ahori powachotsa pamaso pawo. Iwo anawapirikitsa Ahoriwo ndi kuwakhalira pamalo pawo mpaka lero.
23 The Avvim lived in villages as far as Gaza; Caphtorim, who came from Caphtor, destroyed them and settled in their place.). Ndipo za Aavi omwe ankakhala mʼmidzi yofika mpaka ku Gaza, anagonjetsedwa ndi Akafitori wochokera ku Akafitori nakhala pamalo pawo).
24 "Set out and cross the Wadi Arnon. Look, I have given Sihon the Amorite, king of Heshbon, and his land into your hand. Begin to take possession—engage him in battle. “Tsopano nyamukani, muwoloke khwawa la Arinoni. Taona ndapereka mʼmanja mwako Sihoni Mwamori mfumu ya Hesiboni ndi dziko lake lonse. Yambapo kutenga chuma chake ndi kumenyana naye nkhondo.
25 Today I will begin putting dread and fear of you on every people under heaven. They will hear the report of you, tremble, and writhe in anguish because of you." Lero lomwe lino ndidzayamba kuyika chiopsezo ndi mantha pa mitundu yonse pansi pa thambo kuti akuope. Iwowo adzamva zambiri yako ndipo adzanjenjemera ndi kuwawidwa mtima chifukwa cha iwe.”
26 I sent messengers from the wilderness of Kedemoth to Sihon king of Heshbon with words of peace, saying, Ine ndinatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti kupita kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni kukanena mawu ofuna mtendere ndipo ndinati,
27 "Let me pass through your land. I will stay only on the road, turning aside neither right nor left. “Tiloleni tidutse mʼdziko mwanu. Ife tidzangodutsa ndi msewu waukulu, ndipo sitidzapatukira kumanja kapena kumanzere.
28 Sell me food for money to eat, give me water for money to drink—only let me pass through on foot, Mutigulitse chakudya kuti tidye ndi madzi kuti timwe pa mtengo wa siliva. Mungotilola kuti tidutse, tikuyenda pansi
29 as Esau's descendants who live in Seir and the Moabites who live in Ar did for me, until I cross the Jordan into the land our Father is giving us." monga mmene anatichitira adzukulu a Esau okhala ku Seiri ndi Amowabu okhala ku Ari mpaka titawoloka Yorodani kufika ku dziko limene Yehova Mulungu wathu akutipatsa.”
30 But Sihon king of Heshbon refused to let us pass, for our Father hardened his spirit and stiffened his heart, to hand him over to you, as he has done this day. Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanalole kuti tidutse. Popeza Yehova Mulungu wanu analimbitsa mzimu wake, nawumitsa mtima wake kuti amupereke mʼmanja mwanu monga wachitira lero lino.
31 And our Father said to me, "Look, I've begun giving you Sihon and his land. Begin now taking possession—possess his land." Yehova anati kwa ine, “Taona ndayamba kumupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Tsopano yamba kugonjetsa ndi kulanda dziko lake.”
32 Then Sihon came out against us, he and all his people, to fight at Jahaz. Sihoni ndi ankhondo ake atabwera kudzakumana nafe mwankhondo pa Yahazi,
33 And our Father gave him to us, and we struck him down, his sons, and all his people. Yehova Mulungu anamupereka iye kwa ife ndipo tinankantha, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse lankhondo.
34 At that time we captured all his cities and completely destroyed every city—men, women, children—leaving no survivor. Pa nthawi imeneyi tinamulanda mizinda yake yonse ndi kuyiwononga kwathunthu, amuna, akazi ndi ana. Palibe amene anapulumuka.
35 We plundered only the livestock for ourselves, plus the spoil of the cities we captured. Koma ziweto ndi zinthu zonse zimene tinalanda mʼmizinda imene tinagonjetsayo, tinazitenga kukhala zathu.
36 From Aroer on the Wadi Arnon's edge, and from the town in the valley, to Gilead, no town was too strong for us; Our Father gave them all to us. Kuchokera ku Aroeri mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni ndi ku mzinda wa ku mtsinjeko mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe ndi mzinda ndi umodzi omwe umene unatikanika kuwugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anatipatsa onsewo.
37 But you did not go near the Ammonites' land, all along the banks of the Wadi Jabbok and the hill country's towns, just as our Father commanded us. Molingana ndi lamulo la Yehova Mulungu wathu, simunalowerere dziko lililonse la Aamoni, ngakhale dera lonse la ku mtsinje wa Yaboki kapena dera lozungulira dera la ku mizinda ya ku mapiri.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]