1Then the high priest asked, "Are these things true?"OCCLKenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?”
2Stephen said, "Brothers and fathers, listen: Our Father of glory appeared to our father Abraham in Mesopotamia, before he lived in Haran,OCCLStefano anayankha kuti, “Abale ndi makolo, tamverani! Mulungu waulemerero anaoneka kwa kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani.
3and told him, 'Leave your land and relatives, and go to the land I'll show you.'OCCLMulungu anati, ‘Tuluka mʼdziko lako, siya abale ako, ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.’
4He left the Babylonians' land and settled in Haran. After his father died, our Father moved him from there into this land you now live in.OCCL“Ndipo iye anatulukadi mʼdziko la Akaldeya ndi kukakhala ku Harani. Atamwalira abambo ake, Mulungu anamuchotsa kumeneko ndi kumubweretsa mʼdziko lino limene inu mukukhalamo tsopano.
5He gave him no inheritance in it, not even a foot of ground—yet promised it to him and his descendants after him as a possession, though he had no child.OCCLMulungu sanamupatse cholowa kuno, ngakhale kadera kakangʼono kadziko. Koma Mulungu anamulonjeza kuti adzapereka dziko lino kwa iye ndi kwa zidzukulu zake, ngakhale kuti pa nthawi imeneyi analibe mwana.
6And our Father said his offspring would be foreigners in a land not their own, enslaved and mistreated 400 years.OCCLMulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’
7'I will judge the nation they serve,' our Father said, 'and after, they will come out and worship me in this place.'OCCLMulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’
8He gave him the covenant of circumcision. Abraham fathered Isaac and circumcised him on the eighth day; Isaac fathered Jacob, and Jacob the twelve ancestors.OCCLKenaka Mulungu anachita pangano la mdulidwe ndi Abrahamu. Ndipo Abrahamu, anabereka Isake, namudula ali ndi masiku asanu ndi atatu. Ndipo Isake anabereka Yakobo, Yakobo anabereka makolo khumi ndi awiri aja.
9The ancestors, jealous of Joseph, sold him into Egypt, but our Father was with him,OCCL“Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye
10and rescued him from all his troubles, gave him favor and wisdom before Pharaoh king of Egypt, who made him ruler over Egypt and Pharaoh's whole household.OCCLndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.
11A famine and great suffering struck all Egypt and Canaan, and our fathers found no food.OCCL“Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya.
12Hearing there was grain in Egypt, Jacob sent our fathers there first.OCCLPamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba.
13On the second visit, Joseph made himself known to his brothers, and Pharaoh learned of Joseph's family.OCCLPa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe.
14And Joseph sent for his father Jacob and all his relatives, seventy-five persons in all.OCCLIzi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75.
15And Jacob went down into Egypt, and he died, he and our fathers.OCCLMotero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira.
16They were taken back to Shechem, and buried in the tomb Abraham had bought for silver from Hamor's sons in Shechem.OCCLMitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.
17As the time of the promise our Father gave Abraham neared, the people grew and multiplied in Egypt,OCCL“Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto.
18until there arose over Egypt another king who did not know Joseph.OCCLPambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto.
19This king exploited our people and mistreated our fathers, forcing them to abandon their infants to die.OCCLMfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.
20At that time Moses was born, beautiful in our Father's sight. He was raised three months in his father's house.OCCL“Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu.
21And when he was abandoned, Pharaoh's daughter adopted him and brought him up as her own son.OCCLAtakamutaya, mwana wamkazi wa Farao anamutola nakamulera ngati mwana wake.
22Moses was trained in all Egyptian wisdom, and was strong in speech and action.OCCLMose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto, ndipo anali wamphamvu mʼmawu ndi ntchito zake.
23When he was forty years old, he decided to visit his brothers, the sons of Israel.OCCL“Mose ali ndi zaka makumi anayi, anaganizira zokayendera abale ake Aisraeli.
24Seeing one of them wronged, he defended the oppressed man and avenged him by striking down the Egyptian.OCCLIye ataona mmodzi wa iwo akuzunzidwa ndi Mwigupto, anatchinjiriza Mwisraeliyo, namupha Mwiguptoyo.
25He thought his brothers would understand our Father was giving them salvation through his hand, but they didn't understand.OCCLMose anaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu anamuyika kuti awapulumutse koma iwo sanazindikire.
26The next day he came upon them as they were fighting and tried to reconcile them, saying, 'Men, you are brothers. Why do you wrong each other?'OCCLMmawa mwake Mose anaona Aisraeli awiri akukangana. Iye anayesa kuwayanjanitsa ponena kuti, ‘Amuna inu, ndinu abale; chifukwa chiyani mukufuna kupwetekana?’
27But the man wronging his neighbor shoved Moses aside, saying, 'Who made you ruler and judge over us?OCCL“Koma munthu amene amavutitsa mnzakeyo anakankha Mose ndipo anati, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza.
28Do you want to kill me as you killed the Egyptian yesterday?'OCCLKodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja dzulo?’
29At this word, Moses fled and lived as a foreigner in the land of Midian, where he fathered two sons.OCCLMose atamva mawu awa anathawira ku Midiyani, kumene anakhala mlendo ndipo anabereka ana amuna awiri.
30Forty years later, an angel appeared to him in the wilderness of Mount Sinai, in a burning bush's flame.OCCL“Ndipo patapita zaka makumi anayi mngelo anaonekera kwa Mose mʼmalawi amoto pa chitsamba mʼchipululu pafupi ndi Phiri la Sinai.
31Moses saw it and was amazed; as he approached to look closer, our Father's voice came:OCCLIye ataona zimenezi, anadabwa. Akupita kuti akaonetsetse pafupi, Mose anamva mawu a Ambuye:
32'I am the God of your fathers—the God of Abraham, Isaac, and Jacob.' Moses trembled, not daring to look.OCCL‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.’ Mose ananjenjemera chifukwa cha mantha ndipo sanalimbe mtima kuyangʼananso.
33Then our Father told him, 'Take the sandals off your feet, for the place you're standing on is holy ground.'OCCL“Ndipo Ambuye anati kwa Mose, ‘Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.
34I have indeed seen my people's suffering in Egypt, heard their groaning, and come down to rescue them. Now go—I'm sending you to Egypt.OCCLIne ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse. Tsopano tiye ndikutume ku Igupto.’
35This Moses, whom they rejected, saying, 'Who made you ruler and judge?'—this is the one our Father sent as both ruler and redeemer, through the hand of the angel who appeared to him in the bush.OCCL“Uyu ndi Mose yemwe uja amene Aisraeli anamukana ndi kunena kuti, ‘Ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza?’ Iyeyo anatumidwa ndi Mulungu mwini kuti akakhale wowalamulira ndiponso mpulumutsi, mothandizidwa ndi mngelo amene anamuonekera pa chitsamba.
36This man led them out, doing wonders and signs in the land of Egypt, at the Red Sea, and in the wilderness for forty years.OCCLIye anawatulutsa mu Igupto ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro zozizwitsa mu Igupto, pa Nyanja Yofiira, ndiponso mʼchipululu kwa zaka makumi anayi.
37This is the Moses who told Israel's sons, 'Our Father will raise up a prophet like me for you, from your brothers.'OCCL“Uyu ndi Mose uja amene anati kwa Aisraeli, ‘Mulungu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine.’
38This is the one who was in the wilderness assembly with the angel speaking to him at Mount Sinai, and with our fathers—he received living words to give us.OCCLIyeyu anali mʼgulu la Aisraeli mʼchipululu pamodzi ndi mngelo amene anamuyankhula pa phiri la Sinai ndiponso makolo athu; ndipo Mose analandira mawu amoyo kuti atipatse ife.
39Our fathers refused to obey him; they rejected him and in their hearts turned back to Egypt,OCCL“Koma makolo athu anakana kumumvera iye. Iwo anamukana iye ndipo mʼmitima mwawo anatembenukira ku Igupto.
40telling Aaron, 'Make us gods to go ahead of us. As for this Moses who led us out of the land of Egypt, we don't know what happened to him.'OCCLIwo anati kwa Aaroni, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitsogolera kutuluka mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.
41They made a calf in those days, offered a sacrifice to the idol, and celebrated what their hands had made.OCCLIyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo.
42But our Father turned away, giving them over to worship the host of heaven, as written in the prophets' book: 'Did you bring me slaughtered animals and sacrifices for forty years in the wilderness, house of Israel?OCCLKoma Mulungu anawafulatira, nawapereka kuti apembedze zolengedwa zakumwamba. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la aneneri kuti, “ ‘Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?’
43You carried Moloch's tent and your god Rephan's star, the idols you fashioned to worship them; so I will banish you far beyond Babylon.'OCCLAyi, inu mwanyamula tenti ya Moloki ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene munapanga kuti muziwapembedza. Chifukwa chake, Ine ndidzakutumizani kutali, kupitirira dziko la Babuloni.
44Our ancestors had the tent of witness in the wilderness, as he who spoke to Moses directed him to make it, matching the pattern he'd seen.OCCL“Makolo athu anali ndi tenti ya msonkhano pakati pawo mʼchipululu. Anayipanga monga momwe Mulungu anawuzira Mose, molingana ndi chithunzi chimene Mose anachiona.
45Our fathers in turn brought it in with Joshua when they dispossessed the nations that our Father drove out before them. So it was until the days of David,OCCLMakolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide,
46who found favor with our Father and asked to find a dwelling place for our Father.OCCLamene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo.
47But it was Solomon who built a house for him.OCCLKoma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.
48Yet the Most High does not live in houses made by human hands, as the prophet says:OCCL“Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti,
49'Heaven is my throne, and the earth is my footstool. What kind of house will you build for me, says our Father, or what is the place of my rest?OCCL“ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
50Did not my hand make all these things?'OCCLKodi si dzanja langa linapanga zonsezi?’
51"You stubborn people, uncircumcised in heart and ears, always resist the Holy Spirit—like your fathers, so do you.OCCL“Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera:
52Which of the prophets did your fathers not persecute? They killed those who announced beforehand the Righteous One's coming—whom you have now betrayed and murdered.OCCLKodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye.
53You who received the law through angels and yet did not keep it."OCCLInu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”
54Now when they heard these things they were enraged, and they ground their teeth at him.OCCLAtamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano.
55But Stephen, full of the Holy Spirit, looked into heaven, saw the glory of our Father, and Jesus standing at the right hand of our Father.OCCLKoma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.
56And he said, "Look, I see the heavens opened and the Son of Man standing at our Father's right hand."OCCLStefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”
57But they cried out with a loud voice, covered their ears, and rushed at him.OCCLKoma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye,
58They threw him out of the city and stoned him. The witnesses laid their coats at the feet of a young man named Saul.OCCLanamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo.
59And as they were stoning him, Stephen called out, "Lord Jesus, receive my spirit."OCCLAkumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.”
60Kneeling, he cried out loudly, "Lord, do not hold this sin against them." Then he fell asleep.OCCLNdipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.