Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Acts 26 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Agrippa told Paul, "You may speak for yourself." Then Paul stretched out his hand and began his defense. Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti,
2 King Agrippa, I count myself fortunate to defend myself before you today against all the Jews' accusations, “Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera,
3 especially since you know all Jewish customs and disputes well, so I ask you to hear me out patiently. ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.
4 All Jews know my life from youth, spent from the start among my own nation and in Jerusalem. “Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu.
5 They've long known me, and if willing to testify, that according to our religion's strictest sect I lived as a Pharisee. Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa.
6 And now I stand on trial for hope in the promise our Father made to our fathers. Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu.
7 Our twelve tribes hope to reach this promise, worshiping him fervently night and day. For this hope, king, I am accused by the Jews. Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu.
8 Why is it judged incredible by any of you that our Father raises the dead? Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?
9 I myself thought I must do many things against the name of Jesus of Nazareth. “Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti.
10 That's what I did in Jerusalem: with authority from the chief priests, I locked many of the holy ones in prison, and voted against them when they were being put to death. Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza.
11 In every synagogue I often punished them, trying to force them to speak against God; enraged against them, I hunted them even to foreign cities. Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.
12 On one such journey I went to Damascus with authority and commission from the chief priests. “Pa ulendo wina wotere, ndikupita ku Damasiko ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa akulu a ansembe,
13 At midday, O king, I saw on the road a light from heaven, brighter than the sun, blazing around me and my fellow travelers. Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo.
14 We all fell to the ground, and I heard a voice speaking to me in Hebrew: 'Saul, Saul, why are you persecuting me? It's hard for you to kick against the goads.' Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ”
15 I asked, 'Who are you, Lord?' The Lord said, 'I am Jesus, whom you are persecuting.' Ndipo ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?” Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza.
16 But get up, stand on your feet—I appeared to you for this reason: to appoint you a servant and witness both of what you have seen of me and of what I will yet appear to you, Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa.
17 rescuing you from your people and from the Gentiles—to whom I am sending you, Ine ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu a mtundu wako ndiponso mwa anthu a mitundu ina. Ine ndikukutuma kwa iwo,
18 to open their eyes, so they turn from darkness to light and from Satan's power to our Father, and receive forgiveness of sins and a place among those made holy by faith in me.' kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
19 Therefore, King Agrippa, I was not disobedient to the heavenly vision, “Nʼchifukwa chake Mfumu Agripa, sindinakane kumvera masomphenya wochokera kumwamba.
20 but I declared first to those in Damascus, then in Jerusalem and all the region of Judea, and to the Gentiles too, to repent and turn to our Father, doing deeds that match their repentance. Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko, a ku Yerusalemu, a ku Yudeya konse ndi kwa anthu a mitundu inanso, ndinalalikira kuti akuyenera kulapa ndi kutembenukira kwa Mulungu ndikuti aonetse kulapa kwawo mwa ntchito zawo.
21 For this reason the Jews seized me in the temple and tried to kill me. Ichi nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.
22 With help from our Father, I stand to this day testifying to both small and great, saying nothing beyond what the prophets and Moses said would happen: Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika.
23 that the Christ must suffer, and, first to rise from the dead, proclaim light to both our people and the Gentiles. Iwo ananena kuti Khristu adzamva zowawa ndipo popeza Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalalikira za kuwunika kwa anthu a mtundu wake ndiponso kwa anthu a mitundu ina.”
24 As Paul defended himself, Festus shouted, "Paul, you're insane! Your vast learning is driving you mad." Paulo akudziteteza, Festo anakweza mawu nati, “Wazungulira mutu Paulo! Kuphunzira kwako kwakuchititsa misala.”
25 But Paul said, "I'm not insane, most excellent Festus; I speak words of truth and sound judgment. Paulo anayankha nati, “Wolemekezeka Festo, sindine wozungulira mutu. Zimene ndikunena ndi zoona ndiponso za nzeru.
26 The king knows these things—I speak to him freely. I'm sure none of this escaped him, since it wasn't done in a corner. Mfumu ikuzidziwa bwino zinthu izi, ndipo ndikuyankhula momasuka kwa iyo. Ine ndikukhulupirira kuti palibe kanthu nʼkamodzi komwe kamene sukukadziwa, chifukwa izi sizinachike mseri.
27 King Agrippa, do you believe the prophets? I know that you believe." Mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mawu a aneneri? Ine ndikudziwa kuti mumakhulupirira.”
28 Agrippa said, "So quickly you'd persuade me to be a Christian?" Kenaka Agripa anati kwa Paulo, “Kodi ukuganiza kuti mʼkanthawi kochepa kotere ungandikope kuti ndikhale Mkhristu?”
29 Paul said, "Whether short or long, I pray to our Father that not only you but all who hear me today might become as I am—except these chains." Paulo anayankha kuti, “Ngakhale kanthawi kochepa kapena nthawi yayitali, ine ndikupempha kwa Mulungu kuti osati inu nokha koma aliyense amene akundimva lero lino akhale monga ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”
30 Then the king rose, and the governor and Bernice and those seated with them. Mfumu inayimirira pamodzi ndi bwanamkubwa ndi Bernisi ndiponso anthu onse amene anakhala nawo pamodzi.
31 As they left, they told each other, "This man deserves neither death nor imprisonment." Inatuluka mʼchipindamo, ndipo pamene imayankhula inati, “Munthu uyu sanachite kanthu koyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”
32 Agrippa told Festus, "This man could have been freed if he hadn't appealed to Caesar." Agripa anati kwa Festo, “Munthu uyu akanamasulidwa akanakhala kuti sanapemphe zokaonekera kwa Kaisara.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]