Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

Acts 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 When the day of Pentecost arrived, they were all together in one place. Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi.
2 Suddenly a sound like a violent, rushing wind came from heaven and filled the entire house where they sat. Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala.
3 What looked like divided tongues of fire appeared and rested on each one of them. Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo.
4 All were filled with the Holy Spirit and began speaking in other tongues, as the Spirit gave them words to say. Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.
5 At that time devout Jews from every nation under heaven were living in Jerusalem. Ayuda woopa Mulungu ochokera ku mayiko onse a dziko lapansi ankakhala mu Yerusalemu nthawi imeneyi.
6 When this sound rang out, a crowd gathered, confused, since each one heard them speak in his own language. Utamveka mkokomo uja, gulu la anthu linasonkhana. Anthuwo anadabwa chifukwa aliyense anawamva atumwiwo akuyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana.
7 They were amazed and astonished, saying, "Are not all these who are speaking Galileans? Mothedwa nzeru anafunsana kuti, “Kodi anthu onse amene akuyankhulawa si Agalileya?
8 How is it, then, that each of us hears them in our own native language? Nanga bwanji aliyense wa ife akuwamva iwo mu chinenero cha kwawo?
9 Parthians, Medes, and Elamites; those who live in Mesopotamia, Judea and Cappadocia, Pontus and Asia, Apanti, Amedi ndi Aelami; okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya,
10 Phrygia, Pamphylia, Egypt, the parts of Libya near Cyrene; visitors from Rome, Jews and converts to Judaism; ku Frugiya ndi Pamfiliya, ku Igupto ndi ku madera a ku Libiya kufupi ndi ku Kurene; alendo ochokera ku Roma,
11 Cretans and Arabs—we hear them telling in our own tongues the mighty works of our Father!" Ayuda ndi otsatira chipembedzo cha Chiyuda onse pamodzi; Akrete ndi Aarabu, ife tonse tikuwamva akuyankhula za ntchito zodabwitsa za Mulungu mu ziyankhulo zathu.”
12 They were all amazed and perplexed, saying to one another, "What does this mean?" Modabwa ndi mothedwa nzeru anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Zimenezi zikutanthauzanji?”
13 But others mocked and said, "They are full of sweet wine." Koma ena anawaseka nati, “Aledzera vinyo watsopano.”
14 But Peter stood with the eleven, raised his voice, and declared to them: "Men of Judea, everyone living in Jerusalem—know this and listen carefully to my words. Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena.
15 These people are not drunk, as you suppose, for it is only nine o'clock in the morning. Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa!
16 No, this is what was spoken through the prophet Joel: Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17 'And in the last days, says our Father, I will pour out my Spirit on all people; your sons and your daughters will prophesy, your young men will see visions, and your old men will dream dreams. “ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, anyamata anu adzaona masomphenya, nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18 Even on my male servants and my female servants in those days I will pour out my Spirit, and they will prophesy. Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo, ndipo iwo adzanenera.
19 I will show wonders in the heavens above and signs on the earth below—blood and fire and billows of smoke. Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20 The sun will be turned to darkness and the moon to blood, before the great and glorious day of the Lord comes. Dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21 And everyone who calls on the name of the Lord will be saved.'" Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22 "Men of Israel, hear these words: Jesus of Nazareth—a man our Father attested to you through miracles, wonders, and signs our Father did through him among you, as you yourselves know. “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa.
23 This man, handed over by our Father's set plan and foreknowledge, you crucified and killed by the hands of lawless men. Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda.
24 But our Father raised him, freeing him from death's agony, since death could not hold him. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.
25 For David says of him: 'I saw our Father always before me, for he's at my right hand, so I won't be shaken.' Pakuti Davide ananena za Iye kuti, “ ‘Ndinaona Ambuye pamaso panga nthawi zonse. Chifukwa Iye ali kudzanja langa lamanja, Ine sindidzagwedezeka.
26 Therefore my heart was glad and my tongue rejoiced; moreover, my body also will rest in hope. Chifukwa chake mtima wanga ndi wokondwa ndipo lilime langa likukondwera; thupi langanso lidzakhala ndi chiyembekezo.
27 For you will not abandon my soul to the grave, nor let your Holy One see decay. Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda, kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.
28 You have shown me the paths of life; you will fill me with gladness in your presence." Inu munandidziwitsa ine njira zamoyo; Inu mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’
29 "Brothers, I can tell you plainly: our ancestor David died, was buried, and his tomb remains with us to this day. “Abale, ine ndikuwuzani motsimikiza kuti kholo lathu Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda, ndipo manda ake alipo lero lino.
30 Since he was a prophet, he knew our Father had sworn an oath to seat one of his descendants on his throne, Koma iye anali mneneri ndipo anadziwa kuti Mulungu analonjeza ndi lumbiro kuti adzayika mmodzi wa zidzukulu zake pa mpando waufumu.
31 he foresaw and spoke of the Christ's resurrection, that he was not abandoned to the grave, nor his body saw decay. Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole.
32 This Jesus our Father raised up, and we are all witnesses of it. Mulungu wamuukitsa Yesu ameneyu, ndipo ife ndife mboni za zimenezi.
33 So, lifted up to our Father's right hand, having received the promised Holy Spirit from the Father, he poured out what you now see and hear. Khristu anakwezedwa kukhala kudzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera amene Atate anamulonjeza, ndipo watipatsa ife zimene mukuona ndi kumvazi.
34 For David never went up into heaven, but he himself says: "Our Father said to my Lord, 'Sit at my right hand, Pakuti si Davide anakwera kumwamba koma iye akuti, “ ‘Ambuye anawuza Ambuye anga kuti: Khala kudzanja langa lamanja
35 until I make your enemies a footstool for your feet.'" mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.’
36 "So let the whole house of Israel know for certain: our Father made this Jesus, whom you crucified, both Lord and Christ." “Nʼchifukwa chake, Aisraeli onse adziwe ndithu kuti, Yesu amene inu munamupachika, Mulungu wamuyika kukhala Ambuye ndiponso Mpulumutsi.”
37 Cut to the heart at this, they asked Peter and the other apostles, "Brothers, what should we do?" Anthu atamva zimenezi, anatsutsika kwambiri mu mtima ndipo anati kwa Petro ndi atumwi enawo, “Abale, kodi ife tichite chiyani?”
38 Peter said to them, "Repent, and each of you be baptized in the name of Jesus Christ for the forgiveness of your sins, and you will receive the gift of the Holy Spirit. Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
39 For the promise is for you, your children, and all far off—as many as the Sovereign our Father will call to himself." Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.”
40 And with many other words he warned and urged them, saying, "Save yourselves from this corrupt generation." Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.”
41 So those who welcomed his message were baptized, and about 3,000 people were added that day. Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.
42 They devoted themselves to the apostles' teaching and deep communion, to the breaking of bread and the prayers. Iwo ankasonkhana pamodzi kuphunzitsidwa ndi atumwi, pachiyanjano, pachakudya ndi popemphera.
43 Awe came over everyone, and many wonders and signs were done through the apostles. Aliyense ankachita mantha chifukwa cha zodabwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.
44 All who believed were together and had all things in common. Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse.
45 They sold their property and possessions and distributed the proceeds to all, as anyone needed. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake.
46 Every day, devoting themselves together in the temple, breaking bread house to house, they shared food with joyful, sincere hearts, Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.
47 praising our Father, with favor among all the people. The Lord added to their number daily those being saved. Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]