Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

2 Samuel 24 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Again the anger of our Father burned against Israel, and he incited David against them, saying, "Go, take a census of Israel and Judah." Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.”
2 So the king said to Joab, the commander of the army who was with him, "Go now throughout all the tribes of Israel, from Dan to Beersheba, and count the people, so that I may know the number of the people." Choncho mfumu inati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali nawo. “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba kuti mukawerenge anthu omenya nkhondo ndi cholinga choti ndidziwe chiwerengero chawo.”
3 But Joab said to the king, "May your Father add to the people one hundred times as many as they are, and may the eyes of my lord the king see it. But why does my lord the king want to do this thing?" Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?”
4 But the king's command overruled Joab and the commanders of the army. So Joab and the commanders of the army left the king's presence to count the people of Israel. Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli.
5 They crossed the Jordan and camped near Aroer, south of the city that lies in the middle of the valley, toward Gad and on to Jazer. Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri.
6 Then they came to Gilead and to the region of Tahtim-hodshi, and they came to Dan-jaan and around to Sidon, Iwo anapita ku Giliyadi ndi ku chigwa cha Tahitimu Hodisi ndipo anapitirira mpaka ku Dani Yaani ndi madera ozungulira Sidoni.
7 and came to the fortress of Tyre and to all the cities of the Hivites and the Canaanites, and they went out to the Negev of Judah at Beersheba. Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda.
8 So when they had gone through all the land, they came to Jerusalem at the end of nine months and twenty days. Atayendayenda mʼdziko lonse anabwerera ku Yerusalemu patapita miyezi isanu ndi inayi ndi masiku makumi awiri.
9 Joab reported the census count to the king: in Israel there were 800,000 valiant men who drew the sword, and Judah had 500,000. Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa mfumu: Mu Israeli munali anthu 800,000 amphamvu amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga ndipo mu Yuda munali anthu 500,000.
10 But David's heart struck him after he had counted the people. And David said to our Father, "I have sinned greatly in what I have done. Now, my Father, please take away the guilt of your servant, for I have acted very foolishly." Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
11 When David rose in the morning, the word of our Father came to the prophet Gad, David's seer: Davide asanadzuke mmawa mwake mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlosi wa Davide kuti,
12 "Go and say to David, 'This is what our Father says: I am holding three things over you. Choose one of them, and I will carry it out against you.'" “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”
13 So Gad came to David and told him, asking, "Will three years of famine come upon your land? Or will you flee three months before your enemies while they pursue you? Or will there be three days of plague in your land? Now think it over and decide what answer I should bring back to the one who sent me." Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.”
14 Then David said to Gad, "I am in deep distress. Let us fall into the hand of our Father, for his compassion is very great; but do not let me fall into the hand of man." Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.”
15 So our Father sent a plague upon Israel from the morning until the appointed time, and 70,000 of the people from Dan to Beersheba died. Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba.
16 But when the angel stretched out his hand toward Jerusalem to destroy it, our Father relented from the disaster and said to the angel who was destroying the people, "Enough! Now stay your hand." The angel of our Father was then by the threshing floor of Araunah the Jebusite. Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
17 When David saw the angel who was striking the people, he spoke to our Father and said, "Look, I am the one who has sinned; I am the one who has done wrong. But these sheep, what have they done? Please, let your hand fall on me and on my father's house." Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”
18 That day Gad came to David and said to him, "Go up and raise an altar to our Father on the threshing floor of Araunah the Jebusite." Tsiku limenelo Gadi anapita kwa Davide ndi kukanena kuti, “Pitani kamangeni guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.”
19 So David went up, according to the word of Gad, as our Father had commanded. Ndipo Davide anapita monga momwe Yehova anamulamulira kudzera mwa Gadi.
20 When Araunah looked down and saw the king and his servants coming toward him, he went out and bowed before the king with his face to the ground. Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.
21 And Araunah said, "Why has my lord the king come to his servant?" David replied, "To buy the threshing floor from you, to build an altar to our Father, so that the plague may be held back from the people." Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.”
22 Araunah said to David, "Let my lord the king take and offer up whatever seems good to him. Look, here are the oxen for the burnt offering, and the threshing sledges and the ox yokes for the wood. Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni.
23 All this, O king, Araunah gives to the king." And Araunah said to the king, "May the LORD your God accept you." Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.”
24 But the king said to Araunah, "No, I insist on buying it from you for a price. I will not offer to my Father burnt offerings that cost me nothing." So David bought the threshing floor and the oxen for about one.Two pounds of silver. Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu.
25 And David built an altar there to our Father and offered burnt offerings and peace offerings. So our Father responded to the plea for the land, and the plague was held back from Israel. Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]