Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

2 Samuel 22 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 David spoke to our Father the words of this song when our Father rescued him from the hand of all his enemies and from the hand of Saul. Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
2 He said: My Father is my rock, my fortress, my rescuer. Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
3 My Father, my rock, in whom I take refuge, my shield and the power of my salvation, my stronghold and my refuge, my savior—you save me from violence. Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
4 I call upon my Father, who is worthy of praise, and I am saved from my enemies. “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
5 For the waves of death engulfed me; the torrents of destruction terrified me. “Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
6 The cords of the grave entangled me; the snares of death confronted me. Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane.
7 In my distress I called upon my Father; I cried out to my God for help. From his temple he heard my voice, and my cry reached his ears. “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.
8 Then the earth shook and quaked; the foundations of the heavens trembled and shook, because he was angry. “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
9 Smoke rose from his nostrils, and consuming fire came from his mouth; burning coals blazed from him. Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
10 He parted the heavens and came down, with dark clouds beneath his feet. Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
11 He mounted a cherub and flew; he soared on the wings of the wind. Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
12 He made darkness his canopy around him—the dark rain clouds of the skies. Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga.
13 Out of the brightness before him blazed coals of fire. Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera makala amoto alawilawi.
14 My Father thundered from heaven; the Most High raised his voice. Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
15 He shot his arrows and scattered his foes, hurled lightning and routed them. Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
16 The channels of the sea appeared, the foundations of the world were laid bare at the rebuke of my Father, at the blast of breath from his nostrils. Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
17 He reached down from on high and took hold of me; he drew me out of deep waters. “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama.
18 He rescued me from my powerful enemy, from my foes who were too strong for me. Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
19 They confronted me in the day of my disaster, but my Father was my support. Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa.
20 He brought me out into a spacious place; he rescued me because he delighted in me. Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.
21 My Father dealt with me according to my righteousness; according to the purity of my hands he rewarded me. “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
22 For I have kept the ways of my Father; I have not wickedly turned from my God. Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
23 All his judgments are before me; I have not turned aside from his statutes. Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake.
24 I was blameless before him, and I kept myself free from my guilt. Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
25 So my Father rewarded me according to my righteousness, according to my purity in his sight. Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.
26 To the faithful you show yourself faithful; to the blameless you show yourself blameless. “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu, kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
27 To the pure you show yourself pure, but to the crooked you show yourself shrewd. Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
28 You save the afflicted people, but your eyes are on the haughty, to bring them low. Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
29 For you are my lamp, my Father; he turns my darkness into light. Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
30 With you I can charge an army; with my Father I can leap over a wall. Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.
31 As for my Father, his way is perfect; the word of my Father is flawless. He is a shield to all who take refuge in him. “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.
32 For who is God but our Father? And who is a rock except our Father? Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
33 My Father is my strong refuge; he makes my way blameless. Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga.
34 He makes my feet like the feet of a deer and sets me secure on the heights. Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
35 He trains my hands for battle, so that my arms can bend a bow of bronze. Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
36 You have given me the shield of your salvation, and your gentleness has made me great. Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso; mumawerama kuti mundikweze.
37 You widen the path beneath me, so that my ankles do not give way. Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke.
38 I pursued my enemies and destroyed them; I did not turn back until they were finished. “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
39 I consumed them and shattered them so they could not rise; they fell beneath my feet. Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
40 You armed me with strength for battle; you made my adversaries bow beneath me. Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo; munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
41 You made my enemies turn their backs in flight, and those who hated me I destroyed. Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga.
42 They looked, but there was no one to save them—even to my Father, but he gave no answer. Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43 I ground them as fine as the dust of the earth; I crushed and trampled them like mud in the streets. Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.
44 You delivered me from the strife of my people; you kept me as head of nations; a people I did not know now serves me. “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45 Foreigners cower before me; as soon as they hear, they obey me. Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera.
46 Foreigners lose heart; they come trembling from their strongholds. Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
47 My Father lives! Blessed be my Rock! Exalted be my Father, the Rock of my salvation! “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
48 It is my Father who gives me justice and brings peoples down beneath me. Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
49 He brings me out from my enemies. You lifted me high above my foes; you rescued me from the violent man. amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
50 Therefore I will praise you among the nations, my Father; I will sing praises to your name. Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
51 He gives great victories to his king and shows covenant love to his anointed, to David and his descendants forever. “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]