Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

2 Chronicles 2 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 Solomon resolved to build a house for our Father's name, and a royal palace for himself. Solomoni anatsimikiza zoti amange Nyumba ya Dzina la Yehova ndi nyumba yake yaufumu.
2 Solomon assigned 70,000 carriers, 80,000 stonecutters in the mountains, and 3,600 overseers over them. Iye analemba ntchito anthu 70,000 onyamula katundu ndi anthu 80,000 okumba miyala ku mapiri ndiponso akapitawo 3,600 oyangʼanira anthuwo.
3 Solomon sent to Huram king of Tyre: "Deal with me as you did with my father David, sending him cedar to build his house to live in. Solomoni anatumiza uthenga uwu kwa Hiramu mfumu ya ku Turo: “Munditumizire mitengo ya mkungudza monga munachitira ndi abambo anga pamene munawatumizira mitengo ya mkungudza yomangira nyumba yaufumu yokhalamo.
4 I am building a house for the name of my Father, to dedicate it to him—to burn fragrant incense before him, set out the bread of the Presence continually, offer burnt offerings morning and evening, on sabbaths, new moons, and appointed feasts of our Father. Israel must do this forever. Tsono ine ndikufuna kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wanga ndi kuyipereka kwa Iye kuti tiziyikamo buledi wopatulika nthawi zonse ndiponso kuperekeramo nsembe zopsereza mmawa uliwonse ndi madzulo ndi pa masabata ndi pa masiku a chikondwerero cha mwezi watsopano ndiponso pa masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova Mulungu wathu, monga mwa malamulo a Aisraeli mpaka muyaya.
5 The house I am building will be great, for our Father is greater than all gods. “Nyumba ya Mulungu imene ndidzamange idzakhala yayikulu, chifukwa Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.
6 But who can build him a house, when heaven and the highest heavens cannot contain him? And who am I to build him one, except to burn sacrifices before him? Koma ndani angathe kumumangira Iye Nyumba, pakuti mlengalenga, ngakhale kumwamba kwenikweni sikungamukwane? Tsono ine ndine yani kuti ndimangire Iyeyo Nyumba, kupatula malo chabe opserezerapo nsembe pamaso pake?
7 Now send me a craftsman skilled in gold, silver, bronze, iron, purple, crimson, and blue yarn, and in engraving, to work with my skilled workers in Judah and Jerusalem, whom my father David provided. “Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, nsalu yapepo ndi yofiira ndi yobiriwira ndiponso waluso losema, kuti adzagwire ntchito mu Yuda ndi Yerusalemu pamodzi ndi anthu aluso amene abambo anga Davide anandipatsa.
8 Send me also cedar, cypress, and red sandalwood from Lebanon, for I know your servants skillfully cut Lebanon's timber; my servants will join yours. “Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, payini ndiponso matabwa a mʼbawa wa ku Lebanoni, pakuti ndikudziwa kuti anthu anu ali ndi luso locheka matabwa kumeneko. Antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu
9 Prepare plenty of timber for me, for the house I am building will be great and wonderful. kuti andipatse matabwa ambiri, chifukwa Nyumba imene ndikumanga iyenera kukhala yayikulu ndi yokongola.
10 For your servants who cut the timber I will give about 125,000 bushels of crushed wheat, 125,000 of barley, 115,000 gallons of wine, and 115,000 of oil." Ine ndidzalipira antchito anu amene adzacheke matabwa matani 1,000 a tirigu wopunthapuntha, matani 2,000 a barele, malita 440,000 a vinyo, ndiponso malita 440,000 a mafuta a olivi.”
11 Huram king of Tyre wrote Solomon: "Because the LORD loves his people, he made you their king." Hiramu, mfumu ya ku Turo, anamuyankha Solomoni pomulembera kalata kuti, “Chifukwa Yehova amakonda anthu ake, wayika iwe kukhala mfumu yawo.”
12 Huram said: "Blessed be the LORD, God of Israel, maker of heaven and earth! He gave King David a wise son with insight and understanding, to build a house for the LORD and a royal palace for himself. Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti, “Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.
13 Now I am sending you a skilled craftsman, gifted with understanding, Huram-abi, “Ine ndikukutumizira Hiramu Abi, munthu wa luso lalikulu,
14 son of a woman of Dan's daughters, his father a man of Tyre—skilled in gold, silver, bronze, iron, stone, wood, purple, blue, and crimson yarn, and fine linen. He can do any engraving and carry out any design assigned to him, working with your craftsmen and those of my lord David, your father. amene amayi ake anali wochokera ku Dani ndipo abambo ake anali a ku Turo. Iye anaphunzitsidwa kugwira ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, miyala yokongola ndi matabwa, ndiponso nsalu zofewa zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Alinso ndi luso la zosemasema ndipo atha kupanga chilichonse chimene wapatsidwa. Iye adzagwira ntchito ndi amisiri anu ndi a mbuye wanga, Davide abambo anu.
15 So let my lord send his servants the wheat, barley, oil, and wine he promised, “Tsono mbuye wanga tumizirani antchito anu tirigu ndi barele, mafuta a olivi ndi vinyo zimene mwalonjeza,
16 and we'll cut all the timber you need from Lebanon, float it to you as rafts by sea to Joppa, and you can haul it up to Jerusalem." ndipo ife tidzadula mitengo yonse imene mukuyifuna kuchokera ku Lebanoni ndipo tidzayimanga pamodzi ndi kuyiyadamitsa pa madzi mpaka ku Yopa. Ndipo inu mudzatha kuyitenga mpaka ku Yerusalemu.”
17 Solomon counted all the foreigners residing in the land of Israel, as his father David had; they numbered 153,600. Solomoni anawerenga alendo onse amene anali mu Israeli, potsatira chiwerengero chimene abambo ake Davide anachita ndipo panapezeka kuti analipo anthu 153,600.
18 He assigned 70,000 as carriers, 80,000 as stonecutters in the mountains, and 3,600 as overseers to keep the people working. Iye anayika anthu 70,000 kuti akhale onyamula katundu ndi anthu 80,000 kuti akhale ophwanya miyala mʼmapiri, anthu 3,600 anawayika kukhala akapitawo oyangʼanira anthu pa ntchitoyo.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]