Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 27 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 This is the count of Israel's people—heads of families, commanders of thousands and hundreds, and officers serving the king in every matter of the divisions that rotated monthly through the year, each division 24,000. Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
2 Over the first division, for the first month, was Jashobeam son of Zabdiel; his division numbered 24,000. Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
3 He was a descendant of Perez, chief of all army commanders for the first month. Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.
4 Dodai the Ahohite led the second month's division; Mikloth was its chief officer—24,000 men. Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
5 Third army commander, for the third month: Benaiah son of Jehoiada the priest, chief; his division: 24,000. Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000.
6 This Benaiah was the mighty man of the thirty and their leader; his son Ammizabad led his division. Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.
7 Fourth, for the fourth month: Asahel, Joab's brother, then his son Zebadiah; his division: 24,000. Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
8 The fifth, for the fifth month, was the commander Shamhuth the Izrahite; his division numbered 24,000. Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
9 The sixth, for the sixth month, was Ira son of Ikkesh the Tekoite; his division numbered 24,000. Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
10 Seventh, for month seven: Helez the Pelonite, of Ephraim's descendants; his division: 24,000. Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
11 The eighth, for the eighth month, was Sibbecai the Hushathite, of the Zerahites; his division numbered 24,000. Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000
12 The ninth, for the ninth month, was Abiezer the Anathothite, of the Benjamites; his division numbered 24,000. Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
13 The tenth, for the tenth month, was Maharai the Netophathite, of the Zerahites; his division numbered 24,000. Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
14 Eleventh, for month eleven: Benaiah the Pirathonite, from Ephraim's descendants; his division: 24,000. Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
15 Twelfth, for the twelfth month: Heldai the Netophathite, of Othniel's clan; 24,000 in his division. Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.
16 Over the tribes of Israel: Reubenites' leader was Eliezer son of Zichri; Simeonites' leader, Shephatiah son of Maacah, Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa: Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri; mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;
17 for Levi, Hashabiah son of Kemuel; for Aaron, Zadok; mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli, mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;
18 for Judah, Elihu, one of David's brothers; for Issachar, Omri son of Michael; mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide; mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;
19 for Zebulun, Ishmaiah son of Obadiah; for Naphtali, Jerimoth son of Azriel; mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya; mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;
20 for Ephraim's descendants, Hoshea son of Azaziah; for the half-tribe of Manasseh, Joel son of Pedaiah, mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;
21 for the half-tribe of Manasseh in Gilead, Iddo son of Zechariah; for Benjamin, Jaasiel son of Abner; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya; mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;
22 for Dan, Azarel son of Jeroham. These were the leaders of the tribes of Israel. mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu. Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.
23 David did not count those twenty years old and under, since our Father promised to make Israel as many as heaven's stars. Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga.
24 Joab son of Zeruiah started counting but didn't finish; anger came on Israel over it, so the total never appeared in King David's record. Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.
25 Azmaveth son of Adiel oversaw the king's treasuries, and Jonathan son of Uzziah oversaw the storehouses in the fields, towns, villages, and towers. Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.
26 Over the field workers who tilled the soil was Ezri son of Chelub. Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.
27 Shimei the Ramathite oversaw the vineyards; Zabdi the Shiphmite oversaw their produce for the wine cellars. Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.
28 Baal-hanan the Gederite oversaw the olive and sycamore-fig trees in the foothills; Joash oversaw the olive oil stores. Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela. Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.
29 Shitrai the Sharonite oversaw herds grazing in Sharon; Shaphat son of Adlai oversaw herds in the valleys. Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni. Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.
30 Over the camels was Obil the Ishmaelite; and over the donkeys was Jehdeiah the Meronothite. Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira. Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.
31 Over the flocks was Jaziz the Hagrite; all these were officials over King David's property. Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi. Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.
32 Jonathan, David's uncle, was a counselor, a man of understanding and a scribe; and Jehiel son of Hachmoni cared for the king's sons. Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.
33 Ahithophel was the king's counselor, and Hushai the Archite was the king's friend. Ahitofele anali phungu wa mfumu. Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu.
34 After Ahithophel: Jehoiada son of Benaiah, and Abiathar. Joab commanded the king's army. Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara. Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]