Skip to content
The Believer's Library

Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa

1 Chronicles 16 OCCL

Show OCCL only
Verse × ×
1 They brought the ark of our Father and set it inside the tent that David had pitched for it, and they offered burnt offerings and peace offerings before our Father. Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu.
2 When David had finished offering the burnt offerings and peace offerings, he blessed the people in the name of our Father. Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.
3 And he distributed to every Israelite, both men and women, a loaf of bread, a date cake, and a raisin cake. Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.
4 He appointed some of the Levites to minister before the ark of our Father, to invoke, to give thanks, and to praise our Father. Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli.
5 Asaph was the chief, and second to him were Zechariah, then Jeiel, Shemiramoth, Jehiel, Mattithiah, Eliab, Benaiah, Obed-edom, and Jeiel, with harps and lyres; and Asaph sounded the cymbals. Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,
6 Benaiah and Jahaziel the priests were to blow the trumpets regularly before the ark of the covenant of our Father. ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.
7 On that day David first appointed Asaph and his brothers to give thanks to our Father: Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:
8 Give thanks to our Father; call upon his name; proclaim his deeds among the peoples! Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
9 Sing to him; sing praises to him; tell of all his wondrous works! Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando; nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.
10 Exult in his holy name; let the hearts of those who seek our Father rejoice! Nyadirani dzina lake loyera; ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.
11 Seek our Father and his strength; seek his presence continually! Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.
12 Remember the wondrous works that he has done, his miracles and the judgments he pronounced. Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita, zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,
13 You children of Israel his servant, you sons of Jacob, his chosen ones! inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.
14 He is our Father; his judgments are in all the earth. Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.
15 Remember his covenant forever, the word he commanded for 1,000 generations, Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse, mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,
16 the covenant he made with Abraham, his sworn oath to Isaac, pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake.
17 which he confirmed to Jacob as a statute, to Israel as an everlasting covenant, Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo, kwa Israeli monga pangano lamuyaya.
18 saying, "To you I will give the land of Canaan as your allotted inheritance." “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani monga cholowa chimene udzachilandira.”
19 When you were few in number, of little importance, and strangers in the land, Ali anthu owerengeka, ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,
20 wandering from nation to nation, from one kingdom to another people, iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina, ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.
21 he allowed no one to oppress them; he rebuked kings on their account, Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze; chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:
22 "Do not touch my anointed ones, and do my prophets no harm!" “Musakhudze odzozedwa anga; musawachitire choyipa aneneri anga.”
23 Sing to our Father, all the earth! Proclaim his salvation day after day. Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi; lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
24 Publish his glorious deeds among the nations; tell every people the amazing things he has done! Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
25 For great is our Father, and most worthy of praise; he is to be feared above all gods. Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.
26 For all the gods of the peoples are idols, but our Father made the heavens. Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba.
27 Splendor and majesty are before him; strength and joy are in his dwelling. Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake; mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.
28 Ascribe to our Father, all families of the peoples, ascribe to our Father glory and strength! Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,
29 Ascribe to our Father the glory due his name; bring an offering and come before him! Worship our Father in the splendor of holiness. perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake; pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.
30 Tremble before him, all the earth! Indeed, the world is firmly established; it will never be moved. Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi! Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
31 Let the heavens be glad, and let the earth rejoice, and let them say among the nations, "Our Father reigns!" Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere; anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”
32 Let the sea roar, and all that fills it; let the fields exult, and everything in them! Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!
33 Then the trees of the forest will sing for joy before our Father, for he comes to judge the earth. Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba, idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova, pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
34 Give thanks to our Father, for he is good; for his covenant love endures forever! Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.
35 Say also: "Save us, our Father; gather us and rescue us from among the nations, that we may give thanks to your holy name and exult in your praise." Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu, mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina, kuti tiyamike dzina lanu loyera, kuti tikutamandeni.”
36 Blessed be our Father, from everlasting to everlasting! Then all the people said, "Amen!" and praised our Father. Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”
37 So David left Asaph and his brothers there before the ark of the covenant of our Father, to minister regularly before the ark as each day required, Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse.
38 and Obed-edom with his sixty-eight brothers; Obed-edom son of Jeduthun and Hosah were to be gatekeepers. Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.
39 And Zadok the priest and his fellow priests served before the tabernacle of our Father at the high place that was at Gibeon, Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni
40 to offer burnt offerings to our Father on the altar of burnt offering regularly, morning and evening, according to all that is written in the law of our Father, which he commanded Israel. kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli.
41 With them were Heman and Jeduthun and the rest of those chosen and designated by name to give thanks to our Father, for his covenant love endures forever. Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
42 Heman and Jeduthun had with them trumpets and cymbals to sound, and instruments for the sacred songs of our Father. The sons of Jeduthun were stationed at the gate. Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.
43 Then all the people departed, each to his home, and David turned to bless his own household. Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.
FHB

Scripture from Father’s Heart Bible™. © 2026 Spirit Media Publishing, the imprint of Spirit Media Inc. All rights reserved. In Divine Voice™ Color, the words spoken by our Father show in blue, the words of the Son in red, and the words of the Spirit in purple.

OCCL

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa · Creative Commons - Attribution-ShareAlike [CC BY-SA]